ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.
Eksodo 17:3 - Buku Lopatulika Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma anthu aja anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangoŵiringulira Mose, kuti “Chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi ana athu ndi zoŵeta zathu?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?” |
ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.
Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamane mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.
Ndipo anthu ambiri osokonezeka anakwera nao; ndi nkhosa ndi ng'ombe, zoweta zambirimbiri.
Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda mu Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa mu Ejipito?
popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;
Mwalowa nao bwanji msonkhano wa Yehova m'chipululu muno, kuti tifere mommuno, ife ndi zoweta zathu?