Eksodo 17:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?” Onani mutuwoBuku Lopatulika3 Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma anthu aja anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangoŵiringulira Mose, kuti “Chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi ana athu ndi zoŵeta zathu?” Onani mutuwo |