Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 17:11 - Buku Lopatulika

Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele anapambana; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke anapambana.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke analakika.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana.

Onani mutuwo



Eksodo 17:11
8 Mawu Ofanana  

Pakuti uta wanga, ndipo lupanga langa silingandipulumutse.


Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.


Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda.


Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.


Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.