Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi.
Eksodo 17:1 - Buku Lopatulika Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Khamu lonse la Aisraele lija lidachoka ku chipululu cha Sini kuja, ndipo linkangoyenda kuchoka pa chigono china mpaka pa chigono chinanso, monga momwe Chauta ankalamulira. Tsono adakamanga mahema ku Refidimu. Kumeneko kunalibe madzi akumwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa. |
Ndipo Mose anatsogolera Israele kuchokera ku Nyanja Yofiira, ndipo anatulukako nalowa m'chipululu cha Suri; nayenda m'chipululu masiku atatu, osapeza madzi.
Ndipo anachoka ku Elimu, ndi khamu lonse la ana a Israele linalowa m'chipululu cha Sini, ndicho pakati pa Elimu ndi Sinai, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachiwiri atatuluka m'dziko la Ejipito.
Pakuti anachoka ku Refidimu, nalowa m'chipululu cha Sinai, namanga tsasa m'chipululumo; ndipo Israele anamanga tsasa pamenepo pandunji paphirilo.
Ndipo pokwera mtambo kuchokera kuchihema, utatero ana a Israele amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israele amamanga mahema ao.
Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose.