Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 17:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Khamu lonse la Aisraele lija lidachoka ku chipululu cha Sini kuja, ndipo linkangoyenda kuchoka pa chigono china mpaka pa chigono chinanso, monga momwe Chauta ankalamulira. Tsono adakamanga mahema ku Refidimu. Kumeneko kunalibe madzi akumwa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:1
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi.


Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai.


Amaleki anabwera ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraeli.


Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo.


Kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa, choncho anthuwo anasonkhana motsutsana ndi Mose ndi Aaroni.


Nthawi ina iliyonse mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso, ndipo paliponse pamene mtambo wayima, Aisraeli ankamangapo misasa.


Molamulidwa ndi Yehova ankamanga misasa yawo ndipo ankasamukanso Yehova akawalamula. Ankamvera lamulo la Yehova kudzera mwa Mose.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa