Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 16:2 - Buku Lopatulika

Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo khamu lonse la ana a Israele linadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo khamu lonse lidadandaulira Mose ndi Aroni m'chipululu muja kuti,

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mʼchipululumo gulu lonse linadandaulira Mose ndi Aaroni

Onani mutuwo



Eksodo 16:2
10 Mawu Ofanana  

Koma asanagone, anthu a m'mzindamo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;


Koma anaiwala ntchito zake msanga; sanalindire uphungu wake:


koma anadandaula m'mahema mwao, osamvera mau a Yehova.


Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu mu Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.


Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda mu Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa mu Ejipito?


Ndipo anthu anadandaulira Mose, ndi kuti, Tidzamwa chiyani?


Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?


ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.


popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, naonongeka ndi woonongayo.