Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.
Eksodo 14:27 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ake mbandakucha; ndipo Aejipito pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aejipito m'kati mwa nyanja. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ake mbandakucha; ndipo Aejipito pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aejipito m'kati mwa nyanja. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Mose adatambalitsa dzanja lake ku nyanja, ndipo m'mene kunkacha, nkuti madziwo akubwerera m'malo mwake. Aejipitowo adayesa kuthaŵa, koma Chauta adaŵabweza momwe m'nyanjamo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo. |
Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.
Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira chikoti, monga m'kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo chibonga chake chidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anachitira Ejipito,
ndi chochitira Iye nkhondo ya Ejipito, akavalo ao, ndi agaleta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;
Ndi chikhulupiriro anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aejipito poyesanso anamizidwa.
Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine mu Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri.
Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la chipangano la Yehova, kutuluka pakati pa Yordani, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a mu Yordani anabwera m'njira mwake, nasefuka m'magombe ake onse monga kale.