Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 14:11 - Buku Lopatulika

Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda mu Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa mu Ejipito?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo anati kwa Mose, Kodi mwatichotsera kuti tikafe m'chipululu chifukwa panalibe manda m'Ejipito? Nchiyani ichi mwatichitira kuti mwatitulutsa m'Ejipito?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adafunsa Mose kuti, “Kodi nchifukwa chakuti ku Ejipito kunalibe malo a manda, kuti inuyo mutifikitse kuchipululu kuno kuti tidzafe? Mwatichita chiyani potitulutsa ku Ejipito?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iwo anafunsa Mose kuti, “Kodi nʼchifukwa chakuti kunalibe manda ku dziko la Igupto kuti iwe utibweretse muno mʼchipululu kuti tidzafe? Chimene watichitachi nʼchiyani, kutitulutsa mʼdziko la Igupto?

Onani mutuwo



Eksodo 14:11
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Israele anati, Chifukwa ninji munandichitira ine choipa chotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?


Ndipo kunakhala pamene Farao adalola anthu amuke, Mulungu sanawatsogolere njira ya dziko la Afilisti, ndiyo yaifupi; pakuti Mulungu anati, Angadodome anthuwo pakuona nkhondo ndi kubwerera m'mbuyo kunka ku Ejipito.


Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m'phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.


ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo.


Pamenepo Mose anabwerera nanka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawachitiranji choipa anthuwa? Mwandituma bwanji?


Ndipo anthu anaipa, namadandaula m'makutu a Yehova; ndipo pamene Yehova anamva anapsa mtima; ndi moto wa Yehova unayaka pakati pao, nunyeketsa ku chilekezero cha chigono.


Ndipo ngati mundichitira chotero, mundiphetu tsopano apa, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, ndisayang'ane tsoka langa.


popeza anthu onse awa amene adaona ulemerero wanga, ndi zizindikiro zanga, ndidazichita mu Ejipito ndi m'chipululu, koma anandiyesa Ine kakhumi aka, osamvera mau anga;


Koma m'mawa mwake khamu lonse la ana a Israele anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.