Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;
Eksodo 12:40 - Buku Lopatulika Ndipo kukhala kwa ana a Israele anakhala mu Ejipito ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kukhala kwa ana a Israele anakhala m'Ejipito ndiko zaka mazana anai kudza makumi atatu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Aisraele adakhalako zaka 430 ku Ejipito kuja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430. |
Ndipo anati kwa Abramu, Dziwitsa ndithu kuti mbeu zako zidzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo zidzatumikira iwo, ndipo iwo adzasautsa izo zaka mazana anai;
Koma iwo adzabweranso kuno mbadwo wachinai: pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.
Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.
Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai.
Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;