Eksodo 12:39 - Buku Lopatulika39 Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201439 Ndipo anaotcha timitanda topanda chotupitsa ta mtanda umene anabwera nao ku Ejipito, popeza sadaikamo chotupitsa; pakuti adawapirikitsa ku Ejipito, ndipo sanathe kuchedwa, kapena kudzikonzeratu kamba. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa39 Adaphika mitanda ya buledi wosafufumitsa wa ufa wokandiratu, yomwe adachoka nayo ku Ejipito kuja. Ufa wabuledi wokandiratuwo unali wosathira chofufumitsira chifukwa anali atapirikitsidwa mwadzidzidzi ku Ejipito kuja. Panalibe nthaŵi yophikira chakudya chao cha kamba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero39 Iwo anapanga buledi wopanda yisiti ndi ufa umene anachoka nawo ku Igupto. Ufawo unalibe yisiti chifukwa anachita kuthamangitsidwa ku Igupto ndipo analibe nthawi yokonzera chakudya chawo. Onani mutuwo |