ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.
Eksodo 12:32 - Buku Lopatulika Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mutenge nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zanu zomwe, monga momwe mudanenera, ndipo muchoke. Mukapemphere kuti nanenso andidalitseko.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tengani ziweto ndi ngʼombe zanu ndipo pitani kapembedzeni Mulungu wanu monga munanenera kuti ine ndidalitsike.” |
ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.
Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.
Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira.
kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake.
Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.
Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.
Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.
Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.