Eksodo 10:26 - Buku Lopatulika26 Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Koma iyai, zoŵeta zathu zidzapita nafe limodzi ndipo sipadzatsala choŵeta nchimodzi chomwe kuno. Tiyenera kukasankha zoŵeta zokapembedzera nazo Chauta, Mulungu wathu. Mpaka tikafike kumeneko, sitingadziŵe zoyenera kuzigwiritsa ntchito popembedza Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Koma ayi, ife tipita ndi ziweto zathu. Palibe chiweto chilichonse chimene chitatsale kuno, popeza tikasankha komweko ziweto zokapembedzera Yehova. Sitingadziwe zimene tikagwiritse ntchito popembedza Yehova mpaka titakafika kumeneko.” Onani mutuwo |