Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:38 - Buku Lopatulika

38 Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

38 Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

38 Esau adapitirirabe kumpempha bambo wakeyo kuti, “Kodi bambo, dalitso muli nalo limodzi lokhali? Tandidalitsaniko nanenso bambo.” Ndipo atatero adayambanso kulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

38 Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:38
8 Mawu Ofanana  

Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.


Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungire ine mdalitso?


Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.


taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.


Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi.


Tsono mithengayo inafika ku Gibea kwa Saulo, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa