Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Tsono Isaki, bambo wakeyo, adamuuza kuti, “Pa malo ako okhalapo sipadzakhala konse chonde, mvula siidzagwa pa minda yako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Tsono Isake abambo ake anamuyankha kuti, “Malo ako okhalapo sadzabala dzinthu, ndipo mvula sidzagwa pa minda yako.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:39
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;


Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba, ndi zonenepa za dziko lapansi, ndi tirigu wambiri ndi vinyo.


Ndipo Esau anati, Zanga zikwanira; mbale wanga, khala nazo zako iwe wekha.


Ndipo za Yosefe anati, Yehova adalitse dziko lake; ndi zinthu zofunikatu za m'mwamba, ndi mame, ndi madzi okhala pansipo;


Ndipo Israele akhala mokhazikika pa yekha; kasupe wa Yakobo; akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo; inde thambo lake likukha mame.


Ndi chikhulupiriro Isaki anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zilinkudza.


Ndi kwa Isaki ndinapatsa Yakobo ndi Esau, ndipo ndinampatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake; koma Yakobo ndi ana ake anatsikira kunka ku Ejipito.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa