Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 11:7 - Buku Lopatulika

Koma palibe galu adzafunyitsira lilime lake ana onse a Israele ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aejipito ndi Aisraele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma palibe galu adzafunyitsira lilime lake ana onse a Israele ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aejipito ndi Aisraele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Koma pakati pa Aisraele, ndi galu yemwe sadzauwa munthu kapena choŵeta chilichonse, kuti mudziŵe kuti Chauta amasiyanitsa Aejipito ndi Aisraele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma pakati pa Aisraeli, ngakhale galu sadzawuwa munthu aliyense kapena chiweto!” Kotero mudzadziwa kuti Yehova ndiye wasiyanitsa pakati pa Igupto ndi Israeli.

Onani mutuwo



Eksodo 11:7
11 Mawu Ofanana  

Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo, ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.


Akapanda kutembenuka munthu, iye adzanola lupanga lake; wakoka uta wake, naupiringidza.


sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m'nyumba zao.


Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.


M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israele, munalibe matalala.


Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?


anthu onse anabwerera kuchigono kwa Yoswa pa Makeda ndi mtendere. Palibe munthu anachitira chipongwe mmodzi yense wa ana a Israele.