Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 10:23 - Buku Lopatulika

23 sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m'nyumba zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 sanaonane, sanaukenso munthu pamalo pake, masiku atatu; koma kwa ana onse a Israele kudayera m'nyumba zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Aejipitowo sankathanso kuwonana, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adachoka pakhomo pake masiku atatu onsewo. Koma Aisraele okha ankakhala koŵala ndithu kuja ankakhalaku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Palibe amene anatha kuona mnzake kapena kuchoka pa khomo pake kwa masiku atatu. Koma kumalo kumene kumakhala Aisraeli kunali kowala.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:23
15 Mawu Ofanana  

nulowa pakati pa ulendo wa Aejipito ndi ulendo wa Aisraele; ndipo mtambo unachita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizane ndi unzake usiku wonse.


Ndipo anafikira masiku asanu ndi awiri atapanda mtsinje Yehova.


Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoze; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.


Pamenepo alembi anati kwa Farao, Chala cha Mulungu ichi; koma mtima wa Farao unalimba, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Ndipo tsiku ilo ndidzalemba malire dziko la Goseni, m'mene mukhala anthu anga, kuti pamenepo pasakhale mizaza; kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova pakati padzikoli.


M'dziko la Goseni mokha, mokhala ana a Israele, munalibe matalala.


Ndipo Yehova adzasiyanitsa pakati pa zoweta za Israele ndi zoweta za Ejipito; kuti kasafe kanthu kalikonse ka ana a Israele.


Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.


Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.


Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.


amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;


Ndipo pamene anafuula kwa Yehova, anaika mdima pakati pa inu ndi Aejipito nawatengera nyanja, nawamiza; ndi maso anu anapenya chochita Ine mu Ejipito; ndipo munakhala m'chipululu masiku ambiri.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa