Eksodo 10:24 - Buku Lopatulika24 Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu aang'ononso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu ang'ononso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Apo Farao adaitana Mose namuuza kuti, “Pitani mukapembedze Chauta. Mupite nawonso akazi anu ndi ana anu omwe. Koma nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zomwe, zidzasungidwa konkuno.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kapembedzeni Yehova. Ngakhale akazi ndi ana anu apite pamodzi ndi inu. Koma musatenge ziweto zanu ndi ngʼombe zanu.” Onani mutuwo |