Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 10:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kuthambo; ndipo munali mdima bii m'dziko lonse la Ejipito masiku atatu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo Mose anatambasulira dzanja lake kuthambo; ndipo munali mdima bii m'dziko lonse la Ejipito masiku atatu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mose adakweza dzanja lake kumwamba, ndipo pa masiku atatu, mudagwa mdima wandiweyani m'dziko lonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Choncho Mose anakweza dzanja lake kumwamba ndipo mdima wandiweyani unaphimba dziko lonse la Igupto kwa masiku atatu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:22
13 Mawu Ofanana  

Iwo akomana ndi mdima pali dzuwa, nayambasa dzuwa lili pakati pamutu monga usiku.


Anatumiza mdima ndipo kunada; ndipo sanapikisane nao mau ake.


Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu.


nadzayang'ana padziko, koma taonani, nkhawa ndi mdima, kuziya kwa nsautso; ndi mdima woti bii udzaingitsidwa.


Ndipo pakukuzima iwe ndidzaphimba thambo, ndi kudetsa nyenyezi zake; ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo, ndi mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.


Ndidzakudetsera miyuni yonse yakuunikira kuthambo, ndi kuchititsa mdima padziko lako, ati Ambuye Yehova.


tsiku la mdima, la mdima wandiweyani, tsiku la mitambo, mitambo yochindikira, ngati m'mbandakucha moyalika pamapiri; mtundu waukulu ndi wamphamvu, panalibe wotere ndi kale lonse, sipadzakhalanso wotere utapita uwu, kufikira zaka za mibadwo yambiri.


Dzuwa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.


Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.


Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinavumbitsira mzinda umodzi mvula, osavumbitsira mzinda wina; munda wina unavumbidwa mvula, ndi m'munda mosavumbidwa mvula munafota.


Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde paphiri; ndi phirilo linayaka moto kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.


Yehova ananena mau awa kwa msonkhano wanu wonse, m'phirimo ali pakati pa moto, pamtambo, pamdima bii, ndi mau aakulu; osaonjezapo kanthu. Ndipo anawalembera pa magome awiri amiyala, nandipatsa awa.


Ndipo wachisanu anatsanulira mbale yake pa mpando wachifumu wa chilombo; ndipo ufumu wake unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwake,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa