ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.
Eksodo 11:1 - Buku Lopatulika Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala mliri umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Ejipito; pambuyo pake adzakulolani muchoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Tsopano ndimlanga kamodzi kokha Farao, pamodzi ndi Aejipito onse. Pambuyo pa chilango chimenechi, adzakulolani kuti muchoke. Zoonadi, akadzakulolani kuti muchoke, adzachita chokupirikitsani kuno. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzalanga Farao pamodzi ndi Aigupto onse ndi mliri umodzi wotsiriza. Zikadzachitika izi iye adzakulolani kuti mutuluke mʼdziko lino. Ndithu pamene azidzakutulutsani adzachita ngati akukuyingitsani. |
ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.
Mundikonzeranso mboni zonditsutsa, ndi kundichulukitsira mkwiyo wanu; nkhondo yobwerezabwereza yandigwera.
Ndipo panakhala pakati pa usiku, Yehova anakantha ana oyamba onse a m'dziko la Ejipito, kuyambira mwana woyamba wa Farao wakukhala pa mpando wachifumu wake kufikira mwana woyamba wa wam'nsinga ali m'kaidi; ndi ana oyamba onse a zoweta.
Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka.
Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.
Pakuti nthawi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziwe kuti palibe wina wonga Ine padziko lonse lapansi.
Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.
Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.
Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.