Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako padziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere padziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.
Eksodo 10:5 - Buku Lopatulika ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaka yonse idzaphimbidwa ndi dzombelo, ndipo nthakayo sidzaoneka konse. Lidzadya zonse zomwe sizidaonongeke ndi matalala aja. Lidzadya mitengo yako yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu. |
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako padziko la Ejipito, lidze dzombe, kuti likwere padziko la Ejipito, lidye zitsamba zonse za m'dziko, ndizo zonse adazisiya matalala.
Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsale chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba zakuthengo, m'dziko lonse la Ejipito.
Chosiya chimbalanga, dzombe lidachidya; ndi chosiya dzombe, chirimamine adachidya; ndi chosiya chirimamine, anoni adachidya.
Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.
Moto unyambita pamaso pao, ndi m'mbuyo mwao litentha lawi la moto; kumaso kwao dziko likunga munda wa Edeni, koma m'mbuyo mwao likunga chipululu chopanda kanthu; palibenso wakuwapulumuka.