Eksodo 10:6 - Buku Lopatulika6 ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo padziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Ndipo nyumba zako, nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, zonse zidzakhala zodzaza ndi dzombe lokhalokha, chinthu chimene atate anu kapenanso makolo anu sadachiwone chibadwire chao.’ ” Tsono Mose adapotoloka nachoka kwa Farao kuja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’ ” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao. Onani mutuwo |