Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 10:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’ ” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo padziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aejipito onse; sanachione chotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, natuluka kwa Farao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndipo nyumba zako, nyumba za nduna zako ndi za anthu ako, zonse zidzakhala zodzaza ndi dzombe lokhalokha, chinthu chimene atate anu kapenanso makolo anu sadachiwone chibadwire chao.’ ” Tsono Mose adapotoloka nachoka kwa Farao kuja.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:6
11 Mawu Ofanana  

Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao.


Kudzakhala kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, kumene sikunachitikepo ndipo sikudzachitikanso.


Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine, kugwada pamaso panga ndi kunena kuti, “Pita iwe ndi anthu ako onse amene akukutsatirawa! Zimenezi zikadzachitika ine ndidzachoka.” Ndipo Mose anachoka kwa Farao atakwiya kwambiri.


Koma ngati suwalola anthu anga kuti apite, Ine ndidzatumiza pa iwe ntchentche zoluma ndi pa nduna zako ndi anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Mʼnyumba za Aigupto mudzadzaza ntchentche zoluma. Ngakhale pa nthaka pamene akhalapo padzadzaza ndi ntchentche zoluma.’ ”


Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo.


Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero.


Matalala anagwa ndipo ziphaliwali zinangʼanima. Inali mphepo ya mkuntho yoopsa kwambiri imene sinakhaleponso mʼdziko lonse la Igupto chiyambire pamene Aigupto anakhala mtundu woyima pa okha.


tsiku la mdima ndi chisoni, tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani. Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri, gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera, gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.


Amakhamukira mu mzinda, amathamanga mʼmbali mwa khoma. Amakwera nyumba ndi kulowamo; amalowera pa zenera ngati mbala.


Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa