Eksodo 10:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo anyamata ake a Farao ananena naye, Ameneyo amatichitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Ejipito laonongeka? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Nduna za Farao zidafunsa Faraoyo kuti, “Kodi munthu ameneyu adzaleka liti kutivuta chotere? Aloleni anthuwo kuti apite, akapembedze Chauta, Mulungu wao. Kodi simukuwona kuti dziko la Ejipito latheratu kuwonongeka tsopano?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Nduna za Farao zinamufunsa kuti, “Kodi munthu uyu adzativutitsa mpaka liti? Aloleni anthuwa apite, kuti akapembedze Yehova Mulungu wawo. Kodi simukuona kuti dziko la Igupto lawonongeka?” Onani mutuwo |