Eksodo 10:15 - Buku Lopatulika15 Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsale chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba zakuthengo, m'dziko lonse la Ejipito. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 Pakuti linakuta nkhope ya dziko lonse kuti dziko linada; ndipo linadya zitsamba zonse za m'dziko, ndi zipatso zonse za mitengo zimene matalala adazisiya; ndipo sipanatsala chabiriwiri chilichonse, pamitengo kapena pa zitsamba za kuthengo, m'dziko lonse la Ejipito. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Lidangophimba nthaka yonse, ndipo nthakayo idada kuti bii chifukwa cha dzombelo. Lidadya kalikonse komera pa nthaka, pamodzi ndi zipatso zam'mitengo zimene matalala adasiyako. Palibe chachiŵisi chilichonse chimene chidatsalako pa mtengo kapena pa chomera chilichonse m'dziko lonse la Ejipito. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Dzombelo linaphimba nthaka yonse mpaka kuoneka kuti bii. Linadya zonse zimene zinatsala nthawi ya matalala, zomera za mʼmunda ndi zipatso. Panalibe chobiriwira chilichonse chimene chinatsala pa mtengo kapena pa chomera chilichonse mʼdziko lonse la Igupto. Onani mutuwo |