M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;
Eksodo 10:14 - Buku Lopatulika Ndipo dzombe linakwera padziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Lidangophimba dziko lonse, ndipo lidakhazikika m'dzikomo. Kuchuluka kwake kwa dzombelo kunali kwakuti nkale lonse dzombe lotero silidaonekepo, ndipo silidzaonekanso. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo. |
M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la mizinda yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;
Ndipo kudzakhala kulira kwakukulu m'dziko lonse la Ejipito, kunalibe kunzake kotere, sikudzakhalanso kunzake kotere.
Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.
Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka.
Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.