Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 10:14 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

14 Ndipo dzombe linakwera padziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo dzombe linakwera pa dziko lonse la Ejipito, ndipo linatera pakati pa malire onse Ejipito, lambirimbiri; lisanafike ili panalibe dzombe lotere longa ili, ndipo litapita ili sipadzakhalanso lotere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Lidangophimba dziko lonse, ndipo lidakhazikika m'dzikomo. Kuchuluka kwake kwa dzombelo kunali kwakuti nkale lonse dzombe lotero silidaonekepo, ndipo silidzaonekanso.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 10:14
13 Mawu Ofanana  

“Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene mdani wazungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera,


Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala, zokolola zawo kwa dzombe.


Kudzakhala kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, kumene sikunachitikepo ndipo sikudzachitikanso.


Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero.


dzombe lilibe mfumu, komatu lonse limakhala mʼmagulumagulu poyenda.


Wawononga mphesa zanga ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu. Wakungunula makungwa ake ndi kuwataya, kusiya nthambi zake zili mbee.


Mudzadzala mbewu zambiri ku munda koma mudzakolola pangʼono, chifukwa dzombe lidzaziwononga.


Magulumagulu a dzombe adzawononga mitengo yanu ndi mbewu za mʼdziko lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa