Eksodo 10:13 - Buku Lopatulika13 Pamenepo Mose analoza ndodo yake padziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Pamenepo Mose analoza ndodo yake pa dziko la Ejipito; ndipo Yehova anaombetsa padziko mphepo ya kum'mawa usana wonse, ndi usiku womwe; ndipo kutacha mphepo ya kum'mawa inadza nalo dzombe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Choncho Mose adakweza ndodo yake kumwamba, ndipo Chauta adautsa mphepo yakuvuma kuti iwombe pa dziko usana ndi usiku womwe. Pamene kunkacha, nkuti ponseponse pali dzombe lokhalokha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Kotero Mose anakweza ndodo yake pa dziko la Igupto, ndipo Yehova anawutsa mphepo ya kummawa imene inawomba pa dziko usana ndi usiku wonse. Mmene kumacha nʼkuti mphepoyo itabweretsa dzombe. Onani mutuwo |