Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.
Eksodo 1:8 - Buku Lopatulika Pamenepo inalowa mfumu yatsopano mu ufumu wa Ejipito, imene siinadziwe Yosefe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo inalowa mfumu yatsopano m'ufumu wa Ejipito, imene siinadziwa Yosefe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake padaloŵa mfumu ina imene sidadziŵe za Yosefe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto. |
Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.
Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;
Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;
Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.
koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mzindawo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.
Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.
Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israele.