Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
Eksodo 1:22 - Buku Lopatulika Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana aamuna onse akabadwa aponyeni m'mtsinje, koma ana aakazi onse alekeni amoyo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Farao analamulira anthu ake onse, ndi kuti, Ana amuna onse akabadwa aponyeni m'nyanja, koma ana akazi onse alekeni amoyo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Farao adalamula anthu ake kuti, “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa mwa Ahebri azimponya mu mtsinje wa Nailo, koma ana onse aakazi aziŵaleka, azikhala moyo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamenepo Farao analamulira anthu ake onse kuti, “Mwana wamwamuna aliyense akabadwa, mukamuponye mu mtsinje wa Nailo, koma wamkazi mulekeni akhale ndi moyo.” |
Ndipo panali zitapita zaka ziwiri zamphumphu, Farao analota; ndipo, taonani, anaima pamtsinje.
Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.
ninati, Pamene muchiza akazi a Ahebri nimuwaone pamipando; akakhala mwana wamwamuna, mumuphe; akakhala wamkazi, akhale ndi moyo.
Pamene anakavundukula, anapenya mwanayo; ndipo taonani, khandalo lilikulira. Ndipo anamva naye chifundo, nati, Uyu ndiye wa ana a Ahebri.
Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.
Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.
Ndi chikhulupiriro Mose, pobadwa, anabisidwa miyezi itatu ndi akum'bala, popeza anaona kuti ali mwana wokongola; ndipo sanaope chilamuliro cha mfumu.