Ndipo anamdzera kalata yofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayende m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda,
Danieli 5:25 - Buku Lopatulika Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL ndi PARSIN. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UFARSIN. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Mawu amene analembedwa ndi awa: MENE, MENE, TEKELI, PARASINI. |
Ndipo anamdzera kalata yofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayende m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda,
Chifumu chako chatsitsidwa kunsi kumanda, ndi phokoso la mingoli yako; mphutsi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta.
Chifukwa chake choipa chidzafika pa iwe; sudzadziwa kucha kwake, ndipo chionongeko chidzakugwera; sudzatha kuchikankhira kumbali; ndipo chipasuko chosachidziwa iwe chidzakugwera mwadzidzidzi.
Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.
Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao?
Iye anachita zamphamvu ndi mkono wake; Iye anabalalitsa odzitama ndi mlingaliro wa mtima wao.
Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?
Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti.