Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 27:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu akulu adzamuyesa iye mtumiki wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Anthu a mitundu yonse adzamtumikira iyeyo, mwana wake ndi mdzukulu wake, mpaka itakwana nthaŵi yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo anthu a mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzagonjetsa ufumu wakewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:7
29 Mawu Ofanana  

Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.


Katundu wa Babiloni, amene anamuona Yesaya mwana wa Amozi.


ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.


adzanka nazo ku Babiloni, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalo kuno.


Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi mizinda yake yonse, akuti,


Yehova atero: Taonani, ndidzapereka Farao Hofira mfumu ya Aejipito m'manja a adani ake, ndi m'manja a iwo akufuna moyo wake; monga ndinapereka Zedekiya mfumu ya Yuda m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni mdani wake, amene anafuna moyo wake.


Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adzafika adzakantha dziko la Ejipito.


Ndipo panali chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri cha undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namtulutsa iye m'ndende;


Ndipo ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babiloni, ndi kuika lupanga langa m'dzanja lake; koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuula pamaso pake mabuulo a munthu wopyozedwa.


Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemu;


ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.


Sadzauka kodi modzidzimuka iwo amene adzakuluma, ndi kugalamuka iwo amene adzakugwedezetsa; ndipo udzakhala zofunkha zao?


Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.


Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake.


Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa