Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 5:25 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 “Mawu amene analembedwa ndi awa: MENE, MENE, TEKELI, PARASINI.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

25 Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL ndi PARSIN.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UFARSIN.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 5:25
10 Mawu Ofanana  

Yehoramu analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya yonena kuti, “Yehova Mulungu wa Davide abambo ako akuti, ‘Iwe sunayende mʼnjira ya Yehosafati abambo ako kapena Asa mfumu ya Yuda.


Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda, pamodzi ndi nyimbo za azeze ako; mphutsi zayalana pogona pako ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.


Ngozi yayikulu idzakugwera ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako. Mavuto adzakugwera ndipo sudzatha kuwachotsa; chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa chidzakugwera mwadzidzidzi.


Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.


Choncho Iye watumiza dzanja limene lalemba mawu amenewa.


“Zimene mawuwa akutanthauza ndi izi: Mene: Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu ndipo wauthetsa.


Kodi angongole ako sadzakuwukira mwadzidzidzi? Kodi sadzadzuka ndi kukuchititsa mantha? Pamenepo iwe udzalandidwa kalikonse.


Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake; Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.


“Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’


Yehova adzapereka ndithu iweyo pamodzi ndi Aisraeli kwa Afilisti. Ndipo mmawa iweyo ndi ana ako mudzakhala ndi ine kuno. Ndithu Yehova adzapereka gulu lankhondo la Aisraeli kwa Afilisti.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa