Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
Danieli 2:2 - Buku Lopatulika Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Ababiloni, amuululire mfumu maloto ake. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu, |
Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu inkatero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,
Pamenepo Farao anaitananso anzeru, ndi amatsenga; ndipo alembi a Aejipito, iwonso anachita momwemo ndi matsenga ao.
Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.
Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?
Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira. Inawapeza akuposa alembi ndi openda onse mu ufumu wake wonse.
anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.
Ababiloni anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu padziko lapansi wokhoza kuwulula mlandu wa mfumu; chifukwa chake palibe mfumu, mkulu, kapena wolamulira, wafunsira chinthu chotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Ababiloni ali onse.
Nayankha Daniele pamaso pa mfumu, nati, Chinsinsi inachitira liuma mfumu, angakhale anzeru, openduza, alembi, kapena alauli, sangathe kuchiululira mfumu;
Ha! Zizindikiro zake nzazikulu, ndi zozizwa zake nza mphamvu, ufumu wake ndiwo ufumu wosatha, ndi kulamulira kwake ku mibadwomibadwo.
Chifukwa chake ndinalamulira kuti adze kwa ine anzeru onse a ku Babiloni, kuti andidziwitse kumasulira kwake kwa lotoli.
Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.
Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake.