Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 11:17 - Buku Lopatulika

Ndipo adzalimbitsa nkhope yake, kudza ndi mphamvu ya ufumu wake wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzachita chifuniro chake, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kuvomerezana naye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo adzalimbitsa nkhope yake, kudza ndi mphamvu ya ufumu wake wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzachita chifuniro chake, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kuvomerezana naye.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Idzafika ndi mphamvu za ufumu wake wonse ndipo idzayesa kuchita pangano la mtendere ndi mfumu ya kummwera. Ndipo idzamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndi cholinga cholanda ufumu, koma zolinga zake sizidzatheka kapena kumuthandiza.

Onani mutuwo



Danieli 11:17
15 Mawu Ofanana  

Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.


Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.


Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.


Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.


Ndipo Farao ndi nkhondo yake yaikulu, ndi khamu lake launyinji, sadzachita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.


Wobadwa ndi munthu iwe, Lozetsa nkhope yako kwa ana a Amoni, nuwanenere;


Nudzitengere chiwaya chachitsulo, ndi kuchiika ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo; nuulozetsere nkhope yako kuti umangidwire misasa, ndipo udzamangira misasa. Ichi chikhale chizindikiro cha nyumba ya Israele.


Ndipo ulozetse nkhope yako kuzingidwa kwake kwa Yerusalemu, ndi dzanja lako losafundika, nuunenere.


Pamenepo adzatembenuzira nkhope yake kumalinga a dziko lakelake; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso.


Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.


Adzera chiwawa onsewo; nkhope zao zikhazikika zolunjika m'tsogolo; asonkhanitsa andende ngati mchenga.


Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.


Iye wosavomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.


Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe Iye kumwamba, Yesu anatsimikiza kuloza nkhope yake kunka ku Yerusalemu,


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?