Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.
Danieli 10:7 - Buku Lopatulika Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ine Daniele ndekha ndinaona masomphenyawo; pakuti anthu anali nane sanaone masomphenyawo; koma kunawagwera kunjenjemera kwakukulu, nathawa kubisala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine Danieli ndinali ndekha pamene ndinaona masomphenyawa; anthu amene anali ndi ine sanawaone, koma anadzazidwa ndi mantha kotero kuti anathawa ndi kukabisala. |
Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.
Lowa m'phanga, bisala m'fumbi, kuchokera pa kuopsa kwa Yehova, ndi pa ulemerero wachifumu wake.
Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? Ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? Ati Yehova.
Wobadwa ndi munthu iwe, udye mkate wako ndi kunthunthumira, ndi kumwa madzi ako ndi kunjenjemera, ndi kutenga nkhawa;