Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 10:6 - Buku Lopatulika

6 thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 thupi lake lomwe linanga berulo, ndi nkhope yake ngati maonekedwe a mphezi, ndi maso ake ngati nyali zamoto, ndi manja ake ndi mapazi ake akunga mkuwa wonyezimira, ndi kumveka kwa mau ake kunanga phokoso la aunyinji.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Thupi lake linali ngati mwala wonyezimira, nkhope yake ngati chiphaliwali, maso ake ngati muni wowala, manja ndi miyendo yake ngati mkuwa wowala, ndipo mawu ake ngati liwu la chikhamu cha anthu.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 10:6
18 Mawu Ofanana  

ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golide m'zoikamo zao.


Manja ake akunga zing'anda zagolide zoikamo zonyezimira zoti biriwiri. Thupi lake likunga chopanga cha minyanga cholemberapo masafiro.


Ndipo zamoyozo zinathamanga ndi kubwerera, ngati maonekedwe a mphezi yong'anima.


Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.


Ndipo pakuyenda izi ndinamva mkokomo wa mapiko ao, ngati mkokomo wa madzi aakulu, ngati mau a Wamphamvuyonse, phokoso lakusokosera ngati phokoso la ankhondo; pakuima zinagwetsa mapiko ao.


Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.


Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga ina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo.


Ndipo anamuka nane komweko, ndipo taona, panali munthu, maonekedwe ake ngati amkuwa, ndi chingwe chathonje m'dzanja lake, ndi bango loyesa nalo, naima kuchipata iye.


Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, chifaniziro cha maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake, moto; ndi kuyambira m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake, monga maonekedwe a cheza, ngati chitsulo chakupsa.


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


Kuonekera kwake kunali ngati mphezi, ndi chovala chake choyeretsa ngati matalala;


Ndipo m'kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira.


Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;


Ndipo maso ake ali lawi la moto, ndi pamutu pake pali nduwira zachifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha.


Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiatira lemba: Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ake ngati lawi la moto, ndi mapazi ake ngati mkuwa wonyezimira:


achisanu, ndi sardonu; achisanu ndi chimodzi, ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri, ndi krusolito; achisanu ndi chitatu, ndi berulo; achisanu ndi chinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndi achimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri, ndi ametusto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa