Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 3:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo anati, Ndinamva mau anu m'mundamu, ndipo ndinaopa chifukwa ndinali wamaliseche ine; ndipo ndinabisala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Adamu adayankha kuti, “Ndinakumvani m'mundamu ndipo ndinaopa, ndiye ndinabisala ntaona kuti ndili maliseche.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iye anayankha, “Ndinakumvani mʼmundamo, ndipo ndimaopa chifukwa ndinali maliseche; choncho ndinabisala.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 3:10
17 Mawu Ofanana  

Onse awiri ndipo anali amaliseche, mwamuna ndi mkazi wake, ndipo analibe manyazi.


Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?


Ndipo anatseguka maso ao a onse awiri, nadziwa kuti anali amaliseche: ndipo adasoka masamba amkuyu, nadzipangira matewera.


Chifukwa chake ndiopsedwa pankhope pake; ndikalingirira, ndichita mantha ndi Iye.


Ngati ndakwirira zolakwa zanga monga Adamu, ndi kubisa mphulupulu yanga m'chifuwa mwanga;


Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.


Ananenanso, Ine ndine Mulungu wa atate wako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Mose anabisa nkhope yake; popeza anaopa kuyang'ana Mulungu.


Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,


Ochimwa a mu Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?


Maliseche ako adzakhala osafundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzachita kubwezera, osasamalira munthu.


Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kuchita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhale chete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiope Ine konse?


Ndipo tsopano tiferenji? Popeza moto waukulu uwu udzatitha. Tikaonjeza kumva mau a Yehova Mulungu wathu, tidzafa.


m'mene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.


(Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zovala zake, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wake.)


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa