Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Ahebri 8:2 - Buku Lopatulika

Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mtumiki wa malo opatulika, ndi wa chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ai.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Iye akutumikira m'Malo Opatulika am'katikati, ndiye kuti m'chihema chenicheni chimene adachimanga ndi Ambuye osati munthu ai.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.

Onani mutuwo



Ahebri 8:2
15 Mawu Ofanana  

Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha chihema, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange.


Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Ndipo Aroni auvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lake pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakutuluka iye, kuti asafe.


Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,


Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.


amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;


Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo;


ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;


pakuti analindirira mzinda wokhala nao maziko, mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.


Ndipo chingakhale chipangano choyambachi chinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a padziko lapansi.


Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;