Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 2:11 - Buku Lopatulika

11 amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Mwa Iye mudachita ngati kuumbalidwa, osatitu kuumbala kwa anthuku ai, koma kuvula khalidwe lanu lokonda zoipa; kuumbala kumene amachita Khristu nkumeneku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 2:11
22 Mawu Ofanana  

Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala mu Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu.


Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.


Ndipo pamene panakwanira masiku asanu ndi atatu akumdula Iye, anamutcha dzina lake Yesu, limene anatchula mngeloyo asanalandiridwe Iye m'mimba.


Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, Iyeyo ndiye Ambuye, mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja;


Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,


koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu.


podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo;


Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi?


Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.


Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.


Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.


Koma iwo a Khristu Yesu adapachika thupi, ndi zokhumba zake, ndi zilakolako zake.


kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;


Potero dulani khungu la mitima yanu, ndipo musamapulukiranso.


Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.


pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;


Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza, mwa chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,


Pakuti Khristu sanalowe m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu mu Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa