Afilipi 3:11 - Buku Lopatulika ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikuyesetsa kuchita zimenezi pokhulupirira kuti inenso ndidzakhala ndi moyo wosatha podzauka kwa akufa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa. |
ndipo udzakhala wodala; chifukwa iwo alibe chakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa olungama.
Koma pozindikira Paulo kuti ena ndi Asaduki, ndi ena Afarisi, anafuula m'bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.
kufikira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Chifukwa cha chiyembekezo ichi, Mfumu, andinenera Ayuda.
Ndipo popeza dooko silinakome kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera.
kuti ngati nkutheka ndikachititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo.
Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.
Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.
koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
Mwa ichi inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira chikhulupiriro chanu, kuti kapena woyesa akadakuyesani, ndipo chivuto chathu chikadakhala chopanda pake.
munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chafika chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,
chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.
Akazi analandira akufa ao mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa,
Otsala a akufa sanakhalenso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi. Ndiko kuuka kwa akufa koyamba.