Machitidwe a Atumwi 27:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo popeza dooko silinakome kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo popeza dooko silinakoma kugonapo nyengo yachisanu, unyinji unachita uphungu ndi kuti amasule nachokepo, ngati kapena nkutheka afikire ku Fenikisi, ndi kugonako, ndilo dooko la ku Krete, loloza kumpoto ndi kumwera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Tsono popeza kuti dooko silinali labwino kukhalako pa nthaŵi yachisanu, ambiri mwa iwo adafuna kuchokako, nayesa kuti angathe kukafika ku Fenikisi nkukakhala kumeneko pa nthaŵi yachisanu. Fenikisi linali dooko la ku Krete, loloza kumwera chakumadzulo, ndiponso kumpoto chakumadzulo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Popeza kuti dookolo silinali labwino kukhalako nthawi yozizira anthu ambiri anaganiza kuti tichoke. Ife tinkayembekeza kukafika ku Foinikisi ndi kukhala kumeneko nthawi yachisanu. Ili linali dooko la ku Krete, limene limaloza kummwera cha kumadzulo ndiponso kumpoto cha kumadzulo. Onani mutuwo |