Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
Afilipi 1:18 - Buku Lopatulika Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zili nkanthu ngati! Kaya amalalika mwachiphamaso, kaya moona, malinga nkuti Khristu akulalikidwa, pamenepo ine ndikukondwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nanga kodi zimenezo zili ndi ntchito? Chofunika ndi chakuti Khristu alalikidwe, kaya ndi mwachinyengo kapena moona. Ndipo ndikukondwera chifukwa cha chimenechi. Ndithu, ndidzapitirira kukondwera, |
Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.
amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.
Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.
Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.
Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo;
Ndipo chiyani tsono? Tidzachimwa kodi chifukwa sitili a lamulo, koma a chisomo? Msatero ai.
Ndinena chiyani tsono? Kuti choperekedwa nsembe kwa mafano chili kanthu? Kapena kuti fano lili kanthu kodi?
Kuli chiyani tsono? Ndidzapemphera ndi mzimu, koma ndidzapempheranso ndi chidziwitso changa; ndidzaimba ndi mzimu, koma ndidzaimbanso ndi chidziwitso.
Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;