3 Yohane 1:1 - Buku Lopatulika Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'choonadi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mkuluyo kwa Gayo wokondedwayo, amene ndikondana naye m'choonadi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ine mkulune ndikulemba kalatayi kwa Gayo wokondedwa, amene ndimamkonda kwenikweni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndine mkulu wampingo, kulembera: Gayo mnzanga wokondedwa, amene ndimamukonda mʼchoonadi. |
Ndipo m'mzinda monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo.
Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatere mwana wa Piro, wa ku Berea; ndipo a Atesalonika, Aristariko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Deribe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tikiko ndi Trofimo.
Gayo, mwini nyumba wolandira ine, ndi Mpingo wonse wa Ambuye, akupereka moni. Erasto, ndiye woyang'anira mzinda, akupereka moni, ndiponso Kwarto mbaleyo.
Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzavumbulutsikawo:
Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.