Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Mu mzinda wina munali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.
2 Samueli 7:4 - Buku Lopatulika Ndipo kunali usiku womwewo mau a Yehova anafika kwa Natani, kuti, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali usiku womwewo mau a Yehova anafika kwa Natani, kuti, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma usiku womwewo Chauta adauza Natani kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati, |
Ndipo Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Ndipo anafika kwa iye nanena naye, Mu mzinda wina munali anthu awiri; wina wolemera, wina wosauka.
Ndipo Natani anati kwa mfumuyo, Mukani muchite chonse chili mumtima mwanu, pakuti Yehova ali nanu.
Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?
Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga Aisraele m'dziko la Ejipito, sindinasankhe mzinda uliwonse mwa mafuko onse a Israele kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisraele.
Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.
Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.