2 Samueli 7:26 - Buku Lopatulika Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wa makamu ndiye Mulungu wa Israele, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho dzina lanu lidzalemekezedwa mpaka muyaya. Anthu azidzati, ‘Chauta Wamphamvuzonse ndi Mulungu wolamulira Aisraele.’ Tsono banja la ine Davide, mtumiki wanu, lidzakhazikika mpaka muyaya. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu. |
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yake, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimuchite monga munalankhula.
Ndipo kunali, nthawi ya kupereka nsembe yamadzulo, Eliya mneneri anasendera, nati, Yehova Mulungu wa Abrahamu ndi Isaki ndi Israele, lero kudziwike kuti Inu ndinu Mulungu wa Israele, ndi ine mtumiki wanu, kuti mwa mau anu ndachita zonsezi.
Ndimvereni Yehova, ndimvereni, kuti anthu awa adziwe kuti Inu Yehova ndinu Mulungu, ndi kuti Inu mwabwezanso mitima yao.
Kwa ife ai, Yehova, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu patsani ulemerero, chifukwa cha chifundo chanu, ndi choonadi chanu.
Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.
Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.
Atate, lemekezani dzina lanu. Pomwepo adadza mau ochokera Kumwamba, Ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.