2 Samueli 7:27 - Buku Lopatulika27 Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 “Inu, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Aisraele, mwandiwululira ine mtumiki wanu kuti mudzakhazikitsa banja langa. Nchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kuti ndinene pemphero limeneli kwa inu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. Onani mutuwo |
Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.