Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzichepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa.
2 Samueli 6:23 - Buku Lopatulika Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo sanaone mwana kufikira tsiku la imfa yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo sanaone mwana kufikira tsiku la imfa yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mikala, mwana wa Saulo, adaferamo osamuwona mwana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mikala mwana wa Sauli sanakhalenso ndi mwana mpaka anamwalira. |
Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzichepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa.
Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira,
Ndipo Yehova wa makamu wadzivumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu choipa chimenechi sichidzachotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.
Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.
Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.
Ambuye wandichitira chotero m'masiku omwe Iye anandipenyera, kuchotsa manyazi anga pakati pa anthu.
Ndipo Samuele sanadzenso kudzaona Saulo kufikira tsiku la imfa yake; koma Samuele analira chifukwa cha Saulo; ndipo Yehova anali ndi chisoni kuti anamlonga Saulo mfumu ya Israele.