Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 6:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzichepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo ndidzaonjezanso kukhala ngati munthu woluluka, ndidzakhala wodzichepetsa m'maso a ine mwini; ndipo adzakazi udanenawo, ndi amenewo ndidzalemekezedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Ndidzadzinyoza ndithu kupambana pamenepa. Kapena ndidzakhala wonyozeka m'maso mwako, koma m'maso mwa adzakazi amene ukunenawo, ndidzakhala wolemekezeka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Ineyo ndidzadzinyoza kuposa apa, ndipo ndidzakhala wonyozeka mʼmaso mwako. Koma pakati pa akapolo aakazi awa amene umanena za iwo, ndidzalemekezedwa.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 6:22
16 Mawu Ofanana  

sindiyenera zazing'ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwamchitira kapolo wanu: chifukwa ndindodo yanga ndinaoloka pa Yordani uyu; ndipo tsopano ndili makamu awiri.


Koma Davide ananena ndi Mikala, Ndatero pamaso pa Yehova, amene anandisankha ine ndi kupitirira atate wako ndi banja lake lonse, nandiika ndikhale mtsogoleri wa anthu a Yehova, wa Israele, chifukwa chake ndidzasewera pamaso pa Yehova.


Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo sanaone mwana kufikira tsiku la imfa yake.


Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani? Ndigwira pakamwa.


chifukwa chake ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m'fumbi ndi mapulusa.


Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.


Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.


Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.


Ndipo pamene Petro anali pansi m'bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;


Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;


Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.


Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa