2 Samueli 6:12 - Buku Lopatulika Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumzinda wa Davide, ali ndi chimwemwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumudzi wa Davide, ali ndi chimwemwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Davide adamva kuti Chauta wadalitsa banja la Obededomu ndi zinthu zonse zimene anali nazo, chifukwa cha Bokosi lachipangano. Choncho iye adapita kukatenga Bokosi lachipanganolo, kulichotsa m'nyumba ya Obededomu, napita nalo ku mzinda wake, akukondwera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri. |
Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni mu Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mzinda wa Davide, ndiwo Ziyoni.
Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.
Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko zili m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
Momwemo Davide, ndi akuluakulu a Israele, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la chipangano la Yehova, kuchokera kunyumba ya Obededomu mokondwera.
Ndipo Obededomu anali nao ana, woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinai Sakara, wachisanu Netanele,
wachisanu ndi chimodzi Amiyele, wachisanu ndi chiwiri Isakara, wachisanu ndi chitatu Peuletai; pakuti Mulungu adamdalitsa.
Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova kumzinda wa Davide ndiwo Ziyoni.
Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.