Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 8:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adabwera nalo Bokosi la Chautalo, pamodzi ndi chihema chamsonkhano ndiponso ziŵiya zonse zopatulika zimene zinali m'chihemamo. Ansembe ndi Alevi ndiwo amene adabwera nazo zimenezo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 ndipo anabwera nalo Bokosi la Yehova pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula,

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 8:4
5 Mawu Ofanana  

Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumzinda wa Davide, ali ndi chimwemwe.


Ndipo mfumu inapita ku Gibiyoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukulu unali kumeneko, Solomoni anapereka nsembe zopsereza chikwi chimodzi paguwalo la nsembe.


Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.


Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa